4 Cikondi cikhala cilezere, ciri cokoma mtima; cikondi sicidukidwa; cikondi sicidziwa kudzitamanda, sicidzikuza,
5 sicicita zosayenera, sicitsata za mwini yekha, sicipsa mtima, sicilingirira zoipa;
6 sicikondwera ndi cinyengo, koma cikondwera ndi coonadi;
7 cikwirira zinthu zonse, cfkhulupirira zinthu zonse, ciyembekeza zinthu zonse, cipirira zinthu zonse.
8 Cikondi sicitha nthawizonse, koma kapena zonenera zidzakhala cabe, kapena malilime adzaleka, kapena nzeru idzakhala cabe.
9 Pakuti ife tidziwa mderamdera, ndimo tinenera mderamdera.
10 Koma pamene cangwiro cafika, tsono camderamdera cidzakhalacabe.