14 Pakuti ngati ndipemphera m'lilime, mzimu wanga upemphera, koma cidziwitso canga cikhala cosabala kanthu.
15 Kuli ciani tsono? Ndidzapemphera ndi mzimu, koma ndidzapempheranso ndi cidziwitso canga; ndidzayimba ndi mzimu, koma ndidzayimbanso ndi cidziwitso.
16 Cifukwa ngati udalitsa ndi mzimu, nanga iye wakukhala wosaphunzira adzati Amen bwanji, pa kuyamika kwako, popeza sadziwa cimene unena?
17 Pakutitu iwe uyamika bwino, koma winayo samangiriridwa.
18 Ndiyanillca Mulungu kuti ndilankhula malilime koposa inu nonse;
19 koma mu Mpingo ndifuna kulankhula mau asanu ndi cidziwitso canga, kutinso ndikalangize ena, koposa kulankhula mau zikwi m'lilime.
20 Abale, musakhale ana m'cidziwitso, koma m'coipa khalani makanda, koma m'cidziwitso akulu misinkhu.