20 Abale, musakhale ana m'cidziwitso, koma m'coipa khalani makanda, koma m'cidziwitso akulu misinkhu.
21 Kwalembedwa m'cilamulo, Ndi anthu amalilime ena ndipo ndi milomo yina ndidzalankhula nao anthu awa; ndipo kungakhale kutero sadzamva Ine, anena Ambuye.
22 Cotero malilime akhala ngati cizindikilo, si kwa iwo akukhulupira, koma kwa iwo osakhulupira; koma kunenera sikuli kwa iwo osakhulupira, koma kwa two amene akhulupira.
23 Cifukwa cace, ngati Mpingo wonse akasonkhane pamodzi, ndi onse akalankhule malilime, ndipo akalowemo anthu osaphunzira kapena osakhulupira, kodi sadzanena kuti mwayaruka?
24 Koma ngati onse anenera, ndipo alowamo wina wosakhulupirira kapena wosaphunzira, atsutsidwa ndi onse; aweruzidwa ndi onse;
25 zobisika za mtima wace zionetsedwa; ndipo cotero adzagwa nkhope yace pansi, nadzagwadira Mulungu, nadzalalikira kuti Mulungu ali ndithu mwa inu.
26 Nanga ciani tsono, abale? Pamene musonkhana, yense ali nalo salmo, ali naco ciphunzitso, ali nalo bvumbulutso, ali nalo lilime, ali naco cimasuliro. Mucite zonse kukumangirira.