27 Ngati wina alankhula lilime, acite ndi awiri, koma oposa atatu iai, ndipo motsatana; ndipo mmodzi amasulire.
28 Koma ngati palibe womasulira, akhale cete mu Mpingo, koma alankhule ndi iye yekha, ndi Mulungu.
29 Ndipo aneneri alankhule awiri kapena atatu, ndi ena azindikire.
30 Koma ngati kanthu kabvumbulutsidwa kwa wina wakukhalapo, akhale cete woyambayo.
31 Pakuti mukhoza nonse kunenera mmodzi mmodzi, kuti onse aphunzire, ndi onse afulumidwe;
32 ndipo mizimu ya aneneri imvera aneneri;
33 pakuti Mulungu sali Mulungu wa cisokonezo koma wa mtendere; monga mwa Mipingo yonse ya oyera mtima.