28 Koma ngati palibe womasulira, akhale cete mu Mpingo, koma alankhule ndi iye yekha, ndi Mulungu.
29 Ndipo aneneri alankhule awiri kapena atatu, ndi ena azindikire.
30 Koma ngati kanthu kabvumbulutsidwa kwa wina wakukhalapo, akhale cete woyambayo.
31 Pakuti mukhoza nonse kunenera mmodzi mmodzi, kuti onse aphunzire, ndi onse afulumidwe;
32 ndipo mizimu ya aneneri imvera aneneri;
33 pakuti Mulungu sali Mulungu wa cisokonezo koma wa mtendere; monga mwa Mipingo yonse ya oyera mtima.
34 Akazi akhale cete m'Mipingo. Pakuti vsikuloledwa kwa iwo kulankhula, Koma akhale omvera, mongansocilamulo cmena,