37 Ngatiwinaayesa kuti ali mneneri, kapena wauzimu; azindikire kuti zimene ndilemba kwa inu ziri lamulo la Ambuye,
38 Koma ngati wina akhale wosadziwa, akhale wosadziwa.
39 Cifukwa cace; abale anga, funitsitsani kunenera, ndipo musaletse kulankhula malilime.
40 Koma zonse zicitike koyenera ndi kolongosoka.