1 Ndipo ndikudziwitsani, abale, Uthenga Wabwino umene ndinakulalikirani inu, umenenso munalandira, umenenso muimamo,
2 umenenso mupulumutsidwa nao ngati muugwiritsa monga momwe ndinalalikira kwa inu; ngati simunakhulupira cabe.
3 Pakuti ndinapereka kwa inu poyamba, cimenenso ndinalandira, kuti Kristuanafera zoipa zathu, mongamwa malembo;
4 ndi kuti anaikidwa; ndi kutianaukitsidwa tsiku lacitatu, monga mwa malembo;
5 ndi kuti anaonekera kwa Kefa; pamenepo kwa khumi ndi awiriwo;
6 pomwepo anaoneka pa nthawi imodzi kwa abale oposa mazana asanu, amene ocuruka a iwo akhala kufikira tsopano, koma ena agona;