10 Koma ndi cisomo ca Mulungu ndiri ine amene ndiri; ndipo cisomo cace ca kwa ine sicinakhala copanda pace, koma ndinagwirira nchito yocuruka ya iwo onse; koma si ine, komacisomo ca Mulungu cakukhala ndi ine.
11 Ngati ine tsono, kapena iwowa, kotero tilalikira, ndi kotero munakhulupira.
12 Koma ngati Kristu alalikidwa kuti waukitsidwa kwa akufa, nanga ena mwa inu anena bwanjikuti kulibe kuuka kwa akufa?
13 Koma ngati kulibe kuuka kwa akufa, Kristunso sanaukitsidwa;
14 ndipo ngati Kristu sanaukitsidwakulalikira kwathu kuli cabe, cikhulupiriro canunso ciri cabe.
15 Ndiponso ife tipezedwa mboni zonama za Mulungu; cifukwa n tinacita umboni kunena za Mulungu kuti anaukitsa Kristu; amene sanamuukitsa, ngati kuli tero kuti akufa saukitsidwa,
16 Pakuti ngati akufa saukitsidwa, Kristunso sanaukitsidwa;