13 Koma ngati kulibe kuuka kwa akufa, Kristunso sanaukitsidwa;
14 ndipo ngati Kristu sanaukitsidwakulalikira kwathu kuli cabe, cikhulupiriro canunso ciri cabe.
15 Ndiponso ife tipezedwa mboni zonama za Mulungu; cifukwa n tinacita umboni kunena za Mulungu kuti anaukitsa Kristu; amene sanamuukitsa, ngati kuli tero kuti akufa saukitsidwa,
16 Pakuti ngati akufa saukitsidwa, Kristunso sanaukitsidwa;
17 ndipo ngati Kristu sanaukitsidwa, cikhulupiriro canu ciri copanda pace; muli cikhalire m'macimo anu.
18 Cifukwa cace iwonso akugona mwa Kristu anatayika.
19 Ngati tiyembekezera Kristu m'moyo uno wokha, tiri ife aumphawi oposa a anthu onse,