17 ndipo ngati Kristu sanaukitsidwa, cikhulupiriro canu ciri copanda pace; muli cikhalire m'macimo anu.
18 Cifukwa cace iwonso akugona mwa Kristu anatayika.
19 Ngati tiyembekezera Kristu m'moyo uno wokha, tiri ife aumphawi oposa a anthu onse,
20 Koma tsopano Kristu waukitsidwa kwa akufa, cipatso coundukula ca iwo akugona.
21 Pakuti monga imfa inadza mwa munthu, kuuka kwa akufa kunadzanso mwa munthu.
22 Pakuti mongamwa Adamu onse amwalira, coteronso mwa Kristu onse akhalitsidwa ndi moyo.
23 Koma yense m'dongosolo lace la iye yekha, cipatso coundukula Kristu, pomwepo iwo a Kristu, pa kubwera kwace.