26 Mdani wotsiriza amene adzathedwa ndiye imfa.
27 Pakuti Iye anagonjetsa zonse pansi pa mapazi ace. Koma pamene anena kutizonse zagonjetsedwa, kuzindikirika kuti sawerengapo Iye amene anagonjetsa zonsezo kwa Iye.
28 Ndipo pamene zonsezo: zagonjetsedwa kwa iye, pomwepo Mwana yemwe adzagonjetsedwa kwa iye amene anamgonjetsera zinthuzonse; kuti Mulungu akhale zonse mu zonse.
29 Ngati si kutero, adzacita ciani iwo amene abatizidwa cifukwa ca akufa? Ngatiakufa saukitsidwa konse, abatizidwa cifukwa ninji cifukwa ca iwo?
30 Nanga 1 ifenso tiri m'moopsya bwanji nthawi zonse?
31 2 Ndifa tsiku ndi tsiku, ndilumbira pa kudzitamandira kwa inu, abale, kumene ndiri nako mwa Kristu Yesu, Ambuye wathu.
32 3 Ngati odinalimbana ndi zirombo ku Efeso monga mwa munthu, ndipindulanji? Ngati akufa saukitsidwa, 4 tidye timwepakuti mawa timwalira.