3 Pakuti ndinapereka kwa inu poyamba, cimenenso ndinalandira, kuti Kristuanafera zoipa zathu, mongamwa malembo;
4 ndi kuti anaikidwa; ndi kutianaukitsidwa tsiku lacitatu, monga mwa malembo;
5 ndi kuti anaonekera kwa Kefa; pamenepo kwa khumi ndi awiriwo;
6 pomwepo anaoneka pa nthawi imodzi kwa abale oposa mazana asanu, amene ocuruka a iwo akhala kufikira tsopano, koma ena agona;
7 pomwepoanaonekera kwa Yakobo; pamenepo kwa: atumwi onse;
8 ndipo potsiriza pace pa onse, anaoneka kwa inenso monga mtayo.
9 Pakuti ine ndiri wamng'ono wa atumwi, ndine wosayenera kuchedwa mtumwi, popeza ndinalondalonda Eklesia wa Mulungu.