41 Kuli ulemerero wa dzuwa, ndi ulemerero wina wa mwezi, ndi ulemerero wina wa nyenyezi; pakuti nyenyezi isiyana ndi nyenyezi m'ulemerero.
42 9 Comweconso kudzakhala kuuka kwa akufa. Lifesedwa m'cibvundi, liukitsidwa m'cisabvundi;
43 10 lifesedwa m'mnyozo, liukitsidwa m'ulemerero; lifesedwa m'cifoko, liukitsidwa mumphamvu;
44 lifesedwa thupi Iacibadwidwe, liukitsidwa thupi lauzimu. Ngati pali thupi Iacibadwidwe, palinso lauzimu.
45 Koteronso kwalembedwa, 11 Munthu woyamba, Adamu, anakhala mzimu wamoyo. 12 Adamu wotsirizayo anakhala mzimu wakulenga moyo.
46 Koma cauzimu siciri coyamba, koma cacibadwidwe; pamenepo cauzimu.
47 13 Munthu woyambayo ali wapansi, wanthaka. Munthu waciwiri ali wakumwamba.