45 Koteronso kwalembedwa, 11 Munthu woyamba, Adamu, anakhala mzimu wamoyo. 12 Adamu wotsirizayo anakhala mzimu wakulenga moyo.
46 Koma cauzimu siciri coyamba, koma cacibadwidwe; pamenepo cauzimu.
47 13 Munthu woyambayo ali wapansi, wanthaka. Munthu waciwiri ali wakumwamba.
48 14 Monga wanthakayo, ateronso anthaka; ndi monga wakumwamba, ateronso akumwamba.
49 Ndipo 15 monga tabvaia fanizo la wanthakayo, tidzabvalanso fanizo la wakumwambayo.
50 Koma ndinena ici, abale, kuti 16 thupi ndi mwazi sizingathe kulowa Ufumu wa Mulungu; kapena cibvundi sicilowa cisabvundi.
51 Taonani, ndikuuzani cinsinsi; 17 sitidzagona tonse, koma tonse tidzasandulika,