49 Ndipo 15 monga tabvaia fanizo la wanthakayo, tidzabvalanso fanizo la wakumwambayo.
50 Koma ndinena ici, abale, kuti 16 thupi ndi mwazi sizingathe kulowa Ufumu wa Mulungu; kapena cibvundi sicilowa cisabvundi.
51 Taonani, ndikuuzani cinsinsi; 17 sitidzagona tonse, koma tonse tidzasandulika,
52 m'kamphindi, m'kutwanima kwa diso, pa lipenga lotsiriza; pakuti 18 lipenga lidzalira, ndipo akufa adzaukitsidwa osabvunda, ndipoife tidzasandulika.
53 Pakuti cobvunda ici ciyenera kubvala cisabvundi, ndi 19 caimfa ici kubvala cosafa.
54 Ndipo pamene cobvunda ici cikadzabvala cisabvundi ndi caimfa ici cikadzabvala cosafa, pamenepo padzacitika mau olembedwa, 20 Imfayo yamezedwa m'cigonjetso.
55 21 Imfawe, cigonjetso cako ciri kuti? Imfawe, mbola yako iri kuti?