5 ndi kuti anaonekera kwa Kefa; pamenepo kwa khumi ndi awiriwo;
6 pomwepo anaoneka pa nthawi imodzi kwa abale oposa mazana asanu, amene ocuruka a iwo akhala kufikira tsopano, koma ena agona;
7 pomwepoanaonekera kwa Yakobo; pamenepo kwa: atumwi onse;
8 ndipo potsiriza pace pa onse, anaoneka kwa inenso monga mtayo.
9 Pakuti ine ndiri wamng'ono wa atumwi, ndine wosayenera kuchedwa mtumwi, popeza ndinalondalonda Eklesia wa Mulungu.
10 Koma ndi cisomo ca Mulungu ndiri ine amene ndiri; ndipo cisomo cace ca kwa ine sicinakhala copanda pace, koma ndinagwirira nchito yocuruka ya iwo onse; koma si ine, komacisomo ca Mulungu cakukhala ndi ine.
11 Ngati ine tsono, kapena iwowa, kotero tilalikira, ndi kotero munakhulupira.