1 Koma za copereka ca kwa oyera mtima, mongandinalangiza Mipingo ya ku Galatiya, motero citani inunso.
2 Tsiku loyamba la sabata yense wa inu asunge yekha; monga momwe anapindula, kuti zopereka zisacitike pakudza ine.
3 Ndipo pamene ndifika, ndidzatuma iwo amene mudzawayesa oyenera, ndi akalata, apite nayo mphatso yanu ku Yerusalemu.
4 Ndipo ngati kuyenera kwa ine kupitanso, adzapita nane.
5 Koma ndidzadza kwa inu, nditapyola Makedoniya; pakuti ndidzapyola Makedoniya;