1 Ndipo ine, abale, sindinakhoza kulankhula ndi inu manga ndi auzimu, koma monga athupi, monga makanda mwa Kristu.
2 Ndinaiyetsa inu mkaka, si cakudya colimba ai; pakuti simunaeikhoza; ngakhale tsopano lino simucikhoza; pakuti mulinso athupi;
3 pakuti, pokhala pali nkhwidzi ndi ndeu pakati pa inu simuli athupi kodi, ndi kuyendayenda monga mwa munthu?
4 Pakuti pamene wina anena, ine ndine wa Paulo; koma mnzace, Ndine wa Apolo; simuli anthu kodi?