2 Ndinaiyetsa inu mkaka, si cakudya colimba ai; pakuti simunaeikhoza; ngakhale tsopano lino simucikhoza; pakuti mulinso athupi;
3 pakuti, pokhala pali nkhwidzi ndi ndeu pakati pa inu simuli athupi kodi, ndi kuyendayenda monga mwa munthu?
4 Pakuti pamene wina anena, ine ndine wa Paulo; koma mnzace, Ndine wa Apolo; simuli anthu kodi?
5 Ndipo Apolo nciani, ndi Paulo nciani? Atumiki amene munakhulupirira mwa iwo, yense monga Ambuye anampatsa.
6 Ndinanka ine, anathirira Apolo; kama Mulungu anakulitsa.
7 Cotero sali kanthu kapena wookayo, kapena wothirirayo; kama Mulungu amene akulitsa.
8 Koma wookayo ndi wothirirayoali amodzi; koma yense adzalandira mphotho yace ya iye yekha, monga mwa kucititsa kwace kwa iye yekha.