1 Cotero munthu atiyese ife, monga atumiki a Kristu, ndi adindo a zinsinsi za Mulungu.
2 Komatu pano pafunika za adindo, kuti munthu akhale wokhulupirika.
3 Koma kwa ine kuli kanthu kakang'ono ndithu, kuti ndiweruzidwe ndi Inu, kapena pa bwalo la munthu; koma sindiweruza ngakhale ndekha.
4 Pakuti sindidziwa kanthu kakundiparamulitsa; koma m'menemo sindiyesedwa wolungama; koma wondiweruza ine ndiye Ambuye.
5 Cifukwa cace musaweruze kanthu isanadze nthawi yace, kufikira akadze Ambuye, amenenso adzaonetsera zobisika za mdima, nadzasonyeza zitsimikizo za mtima; ndipo pamenepo yense adzakhala nao uyamiko wace wa kwa Mulungu.