3 Koma kwa ine kuli kanthu kakang'ono ndithu, kuti ndiweruzidwe ndi Inu, kapena pa bwalo la munthu; koma sindiweruza ngakhale ndekha.
4 Pakuti sindidziwa kanthu kakundiparamulitsa; koma m'menemo sindiyesedwa wolungama; koma wondiweruza ine ndiye Ambuye.
5 Cifukwa cace musaweruze kanthu isanadze nthawi yace, kufikira akadze Ambuye, amenenso adzaonetsera zobisika za mdima, nadzasonyeza zitsimikizo za mtima; ndipo pamenepo yense adzakhala nao uyamiko wace wa kwa Mulungu.
6 Koma izi, abale, ndadziphiphiritsira ndekha ndi Apolo, cifukwa ca inu, kuti mwa ife mukaphunzire kusapitirira zimene zilembedwa; kuti pasakhale mmodzi wodzitukumulira mnzace ndi kukana wina.
7 Pakuti akusiyanitsa iwe ndani? Ndipo uli naco ciani cosati wacilandira? Koma ngati wacilandira udzitamanda bwanji, monga ngati sunacilandira?
8 M wadzala kale, mwalemerera kale, mwacita ufumu opanda ife; ndipo mwenzi mucitadi ufumu, kuti ifenso tikacite ufumu pamodzi ndi inu.
9 Pakuti ndiyesa, kuti Mulungu anaoneketsa ife atumwi otsiriza, monga titi tife; pakuti takhala ife coonetsedwa ku dziko lapansi, ndi kwa angelo, ndi kwa anthu.