7 Pakuti akusiyanitsa iwe ndani? Ndipo uli naco ciani cosati wacilandira? Koma ngati wacilandira udzitamanda bwanji, monga ngati sunacilandira?
8 M wadzala kale, mwalemerera kale, mwacita ufumu opanda ife; ndipo mwenzi mucitadi ufumu, kuti ifenso tikacite ufumu pamodzi ndi inu.
9 Pakuti ndiyesa, kuti Mulungu anaoneketsa ife atumwi otsiriza, monga titi tife; pakuti takhala ife coonetsedwa ku dziko lapansi, ndi kwa angelo, ndi kwa anthu.
10 Tiri opusa ife cifukwa ca Kristu, koma muli ocenjera inu mwa Kristu; tiri ife ofoka, koma inu amphamvu; inu ndinu olemekezeka, koma ife ndife onyozeka.
11 Kufikira nthawi yomwe yino timva njala, timva ludzu, tid amarisece, tikhomedwa, tiribe pokhazikika;
12 ndipo tigwiritsa nchito, ndi kucita ndi manja athu a ife tokha; polalatidwa tidalitsa; pozunzidwa, tipirira;
13 ponamizidwa, tipempha; takhala monga zonyansa za dziko lapansi, litsiro la zinthu zonse, kufikira tsopano,