1 Kwamveka ndithu kuti kuli cigololo pakati pa inu, ndipo cigololo cotere conga sicimveka mwa amitundu, kuti wina ali naye mkazi wa atate wace.
2 Ndipo mukhala odzitukumula, kosati makamaka mwacita cisoni, kuti acotsedwe pakati pa inu iye amene anacita nchito iyi.
3 Pakuti inedi, thupi langa kulibe, koma mzimu wanga ulipo, ndaweruza kale, monga ngati ndiripo,
4 m'dzina la Ambuye wathu Yesu, posonkhana pamodzi inu ndi mzimu wanga, ndi mphamvu ya Ambuye wathu Yesu,
5 kumpereka iye wocita cotere kwa Satana, kuti lionongeke thupi, kuti mzimu upulumutsidwe m'tsiku la Ambuye Yesu.
6 Kudzitamanda kwanu sikuli bwino. Kodi simudziwa kuti cotupitsa pang'ono citupitsa mtanda wonse?
7 Tsukani cotupitsa cakale, kuti mukakhale mtanda watsopano, monga muli osatupa. Pakutinso Paskha wathu waphedwa, ndiye Kristu;