10 amene anatilanditsa mu imfa yaikuru yotere, nadzalanditsa;
11 amene timyembekezera kuti adzalanditsanso; pothandizana inunso ndi pemphero lanu la kwa ife; kuti pa mphatso ya kwa ife yodzera kwa anthu ambiri, payamikike ndi anthu ambiri cifukwa ca ife.
12 Pakuti kudzitamandira kwathu ndiko umboni wa cikumbu mtima cathu, kuti m'ciyero ndi kuona mtima kwa Mulungu, si m'nzeru ya thupi, koma m'cisomo ca Mulungu tinadzisunga m'dziko lapansi, koma koposa kwa inu.
13 Pakuti sitilemba kwa inu zina, koma zimene muwerenga, kapenanso mubvomereza; ndipo ndiyembekeza kuti mudzabvomereza kufikira cimariziro;
14 monganso munatibvomerezera ife pena, kuti ife ndife kudzitamandira kwanu, monga momwe inunso muli kudzitamandira kwathu m'tsiku la Ambuye wathu Yesu.
15 Ndipo m'kulimbika kumene ndinafuna kudza kwa inu kale, kuti mukakhalenaco cisomo caciwiri;
16 ndipo popyola kwanu kupita ku Makedoniya, ndi kudzanso kwa inu pobwera kufuma ku Makedoniya; ndi kuperekezedwa ndi inu ku Yudeya.