3 Wolemekezeka Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Kristu, Atate wa zifundo ndi Mulungu wa citonthozo conse,
4 woo titonthoza ife m'nsautso yathu yonse, kuti tidzathe ife kutonthoza iwo okhala m'nsautso iri yonse, mwa citonthozo cimene titonthozedwa naco tokha ndi Mulungu.
5 Pakuti monga masautso a Kristu aticurukira ife, coteronso citonthozo cathu cicuruka mwa Kristu,
6 Koma ngati tisautsidwa, kuli cifukwa ca citonthozo ndi cipulumutso canu; ngati titonthozedwa, kuli kwa citonthozo canu cimene cicititsa mwa kupirira kwa masautso omwewo amene ifenso timva.
7 Ndipo ciyembekezo cathu ca kwa inu ncokbazikika; podziwa kuti monga muli oyanjana ndi masautsowo, koteronso ndi citonthozo.
8 Pakuti sitifuna abale, kuti mukhale osadziwa za cisautso cathu tinakomana naco m'Asiya, kuti tinathodwa kwakukuru, koposa mphamvu yathu, kotero kuti tinada nkhawa ngakhale za moyo wathu;
9 koma tokha tinakhala naco citsutso ca imfa mwa ife tokha, kuti tisalimbike pa ife tokha, koma pa Mulungu wakuukitsa akufa;