5 Pakuti ndiyesa kuti sindinaperewera konse ndi atumwi oposatu,
6 Ndipo ndingakhale ndiri wosaphunzira m'manenedwe, koma sinditero m'cidziwitso, koma m'zonse tacionetsa kwa inu mwa anthu onse.
7 Kodi ndacimwa podzicepetsa ndekha, kuti inu mukakwezedwe, popeza ndinalalikira kwa inu Uthenga Wabwino wa Mulungu mwaufulu?
8 ndinalanda za Mipingo yina, ndi kulandira kwa iwo kulipira kuti ndikatumikire inu;
9 ndipo pakukhala nanu, ndi kusowa, sindinasaukitsa munthu ali yense; pakuti abale akucokera ku Makedoniya, anakwaniritsa kusowa kwanga; ndipo m'zonse ndinacenjera ndekha, ndisalemetse inu, ndipo ndidzacenjerapo.
10 Coonadi ca Kristu ciri mwa ine, kuti kudzitamandira kumene sikudzaletsedwa kwa ine mu mbali za Akaya,
11 Cifukwa ninji? Cifukwa sindikonda inu kodi? Adziwa Mulungu.