9 ndipo pakukhala nanu, ndi kusowa, sindinasaukitsa munthu ali yense; pakuti abale akucokera ku Makedoniya, anakwaniritsa kusowa kwanga; ndipo m'zonse ndinacenjera ndekha, ndisalemetse inu, ndipo ndidzacenjerapo.
10 Coonadi ca Kristu ciri mwa ine, kuti kudzitamandira kumene sikudzaletsedwa kwa ine mu mbali za Akaya,
11 Cifukwa ninji? Cifukwa sindikonda inu kodi? Adziwa Mulungu.
12 Koma cimene ndicita, ndidzacitanso, kuti ndikawadulire cifukwa iwo akufuna cifukwa; kuti m'mene adzitamandiramo, apezedwe monganso ife.
13 Pakuti otere ali atumwi onyenga, ocita ocenjerera, odzionetsa ngati atumwi a Kristu,
14 Ndipo kulibe kudabwa; pakuti Satana yemwe adzionetsa ngati mngelo wa kuunika.
15 Cifukwa cace sikuli kanthu kwakukuru ngatinso atumiki ace adzionetsa monga atumiki a cilungamo; amene cimariziro cao cidzakhala monga nchito zao.