1 Ndiyenera kudzitamandira, kungakhale sikupindulika; koma ndidzadza ku masomphenya ndi mabvumbulutso a Ambuye.
2 Ndidziwa munthu wa mwa Kristu, zitapita zaka khumi ndi zinai (ngati m'thupi, sindidziwa; ngati kunja kwa thupi, sindidziwa; adziwa Mulungu), anakwatulidwa wotereyo kunka naye Kumwamba kwacitatu.
3 Ndipo ndidziwa munthu wotereyo (ngati m'thupi, ngati wopanda thupi, sindidziwa; adziwa Mulungu),
4 kuti anakwatulidwa kunka ku Paradaiso, namva maneno osatheka kuneneka, amene saloleka kwa munthu kulankhula.