15 Ndipo ndidzapereka ndi kuperekedwa konse cifucwa ca miyoyo yanu mokondweratu. Ngati ndikonda inu kocuruka koposa, kodi ndikondedwa kocepa?
16 Koma kukhale kotero; ine sindinalemetsa inu; koma pokhala wocenjera ine, ndinakugwirani ndi cinyengo.
17 Kodi wina wa iwo ndinawatuma kwa inu, ndinakucenjererani naye kodi? Ndinadandaulira Tito, ndipo ndinatuma mbaleyo naye.
18 Kodi Tito anakucenjererani kanthu? Sitinayendayenda naye Mzimu yemweyo kodi? Sitinatsata mapazi omwewo kodi?
19 Mumayesa tsopano Uno kuti tirikuwiringula kwa, inu. Tilankhula pamaso pa Mulungu mwa Kristu. Koma zonse, okondedwa, ziri za kumangirira kwanu.
20 Pakuti ndiopa, kuti kaya, pakudza ine, sindidzakupezani inu otere onga ndifuna, ndipo ine ndidzapezedwa ndi inu wotere wonga simufuna; kuti kaya pangakhale cotetana, kaduka, mikwiyo, zilekanitso, maugogodi ukazitape, zodzikuza, mapokoso;
21 kuti pakudzanso ine, Mulungu wanga angandicepse pa inu, ndipo ndingalirire ambiri 1 a iwo amene adacimwa kale, osalapa pa codetsa, ndi cigololo, ndi kukhumba zonyansa zimene anacita.