1 Kodi tirikuyambanso kudzibvomereza tokha? kapena kodi tisowa, monga ena, akalata otibvomerezetsa kwa inu, kapena ocokera kwa inu?
2 Inu ndinu kalata wathu, wolembedwa mu mitima yathu, wodziwika ndi wowerengedwa ndi anthu onse;
3 popeza mwaonetsedwa kuti muli kalata wa Kristu, wakumtumikira ndi ife, wosalembedwa ndi kapezi iai, koma ndi Mzimu wa Mulungu wamoyo; wosatim'magome amiyala, koma m'magome a mitima yathupi.
4 Ndipo kulimbika kotere kwa Mulungu tiri nako mwa Kristu:
5 si kuti tiri okwanira pa ife tokha, kuyesera kanthu monga mocokera mwa ife tokha; kukwanira kwathu kucokera kwa Mulungu;