13 Pakuti ngati tiri oyaruka, titero kwa Mulungu; ngati tiri a nzeru zathu, titero kwa inu.
14 Pakuti cikondi ca Kristu citikakamiza; popeza taweruza cotero, kuti mmodzi adafera onse, cifukwa cace onse adafa;
15 ndipo adafera onse, kuti iwo akukhala ndi moyoasakhalenso ndi moyo kwa iwo okha, koma kwa iye amene adawafera iwo, nauka.
16 Kotero kuti ife sitidziwanso munthu tsopano monga mwa thupi; ndipo ngati tazindikira Kristu monga mwa thupi, koma tsopano sitimzindikiranso motero.
17 Cifukwa cace ngati munthu ali yense ali mwa Kristu ali wolengedwa watsopano; zinthu zakale zapita, taonani, zakhala zatsopano,
18 Koma zinthu zonse zicokera kwa Mulungu amene anatiyanjanitsa kwa iye yekha mwa Kristu, natipatsa utumiki wa ciyanjanitso;
19 ndiko kunena kuti Mulungu anali mwa Kristu, alinkuyanjanitsa dziko lapansi kwa Iyeyekha, osawawerengera zolakwa zao; ndipo anaikiza kwa ife mau a ciyanjanitso,