5 m'mikwingwirima, m'ndende, m'mapokoso, m'mabvutitso, m'madikiro, m'masalo a cakudya;
6 m'mayeredwe, m'cidziwitso, m'cilekerero, m'kukoma mtima, mwa Mzimu Woyera, m'cikondi cosanyenga;
7 m'mau a coonadi, mu mphamvu ya Mulungu; mwa camuna ca cilungamo kulamanja ndi kulamanzere,
8 mwa ulemerero, mwa mnyozo, mwa mbiri yoipa ndi mbiri yabwino; mongaosoceretsa, angakhale ali oona;
9 monga osadziwika, angakhale adziwika bwino; monga alinkufa, ndipo taonani, tiri ndi moyo; monga olangika, ndipo osaphedwa;
10 monga akumva cisoni, koma akukondwera nthawi zonse; monga aumphawi, lroma akulemeretsa ambiri; mensa okhala opanda-kanthu, ndipo akhala nazo zinthu zonse.
11 M'kamwa mwathu mmotseguka kwa inu Akorinto, mtima wathu wakulitsidwa.