5 Pakutinso pakudza ife m'Makedoniya thupi lathu linalibe mpumulo, koma tinasautsidwa ife monsemo; kunjako zolimbana, m'katimo mantha.
6 Koma iye amene atonthoza odzicepetsa, ndiye Mulungu, anatitonthoza ife ndi kufika kwace kwa Tito;
7 koma si ndi kufika kwace kokha, komanso ndi citonthozo cimene anatonthozedwa naco mwa inu, pamene anatiuza ife kukhumbitsa kwanu, kulira kwanu, cangu canu ca kwa ine; kotero kuti ndinakondwera koposa,
8 Kuti ngakhale ndakumvetsani cisoni ndi kalata uja, sindiwawapo mtima, ndingakhale ndinawawa mtima; pakuti ndiona kuti kalata uja anakumvetsani cisoni, ngakhale kwa nthawi yokha.
9 Tsopano ndikondwera, sikuti mwangomvedwa cisoni, koma kuti mwamvetsedwa cisoni ku kutembenuka mtima; pakuti munamvetsedwa cisoni ca kwa Mulungu, kuti tisakusowetseni m'kanthu kali konse.
10 Pakuti cisoni ca kwa Mulungu citembenuzira mtima kueipulumutso, cosamvetsanso cisoni; koma cisonicadziko lapansi cicita imfa.
11 Pakuti, taonani, ici comwe, cakuti mudamvetsedwa cisoni ca kwa Mulungu, khama lalikuru lanji cidalicita mwa inu, komanso codzikonza, komanso mkwiyo, komanso mantha, komanso kukhumbitsa komanso cangu, komanso kubwezera cilango! M'zonse muoadzitsimikizira nokha kuti muli oyera mtima m'menemo.