19 ndipo si ici cokha, komanso anasankhika ndi Mipingo, apite limodzi ndi ife m'cisomo ici, cimene ticitumikira ife, kwa ulemerero wa Ambuye, ndi kuonetsa cibvomerezo cathu;
20 ndi kupewa ici kuti wina angatichule za kucurukira kumene tikutumikira;
21 pakuti tikonzeratu zinthu zokoma, si pamaso pa Ambuye pokha, komanso pamaso pa anthu.
22 Ndipo tinatumiza mbale wathu awaperekeze iwo, amene tamtsimikizirakawiri kawiri ali wakhama m'zinthu zambiri, koma tsopano wa khama loposatu ndi kulimbika kwakukuru kumene ali nako kwa inu,
23 Nanga za Tito, ali woyanjana wanga ndi wocita nane wa kwa inu; nanga abale athu, ali atumwi a Mipingo, ali ulemerero wa Kristu.
24 Cifukwa cace muwatsimikizire iwo citsimikizo ca cikondi canu, ndi ca kudzitamandira kwathu pa inu pamaso pa Mipingo.