6 Kotero kuti tinadandaulira Tito, kuti monga anayamba kale, comweconso atsirize kwa inu cisomo icinso.
7 Koma monga mucurukira m'zonse, m'cikhulupiriro, ndi m'mau, ndi m'cidziwitso, ndi m'khama lonse, ndi m'cikondi canu ca kwa ife, curukaninso m'cisomo ici.
8 Sindinena ici monga kulamulira, koma kuyesa mwa khama la ena coonadi ca cikondi canunso.
9 Pakuti mudziwa cisomo ca Ambuye wathu Yesu Kristu, kuti, cifukwa ca inu anakhala wosauka, angakhale anali wolemera, kuti inu ndi kusauka kwace mukakhale olemera.
10 Ndipo m'menemo odichula coyesa ine; pakuti cimene cipindulira inu, amene munayamba kale caka capitaci si kucita kokha, komanso kufunira.
11 Koma tsopano tsirizani kucitaku; kuti monga kunali cibvomerezo ca kufunira, koteronso kukhale kutsiriza kwacem'cimene muli naco.
12 Pakuti ngati cibvomerezoco ciri pomwepo, munthu alandiridwa monga momwe ali naco, si monga cimsowa.