7 Koma monga mucurukira m'zonse, m'cikhulupiriro, ndi m'mau, ndi m'cidziwitso, ndi m'khama lonse, ndi m'cikondi canu ca kwa ife, curukaninso m'cisomo ici.
8 Sindinena ici monga kulamulira, koma kuyesa mwa khama la ena coonadi ca cikondi canunso.
9 Pakuti mudziwa cisomo ca Ambuye wathu Yesu Kristu, kuti, cifukwa ca inu anakhala wosauka, angakhale anali wolemera, kuti inu ndi kusauka kwace mukakhale olemera.
10 Ndipo m'menemo odichula coyesa ine; pakuti cimene cipindulira inu, amene munayamba kale caka capitaci si kucita kokha, komanso kufunira.
11 Koma tsopano tsirizani kucitaku; kuti monga kunali cibvomerezo ca kufunira, koteronso kukhale kutsiriza kwacem'cimene muli naco.
12 Pakuti ngati cibvomerezoco ciri pomwepo, munthu alandiridwa monga momwe ali naco, si monga cimsowa.
13 Pakuti sinditero kuti ena akamasuke, ndi inu musautsidwe;