37 Inu mfumu ndinu mfumu ya mafumu, pakuti Mulungu wa Kumwamba anakupatsani ufumu, ndi mphamvu yaikuru, ndi ulemu;
38 ndipo pali ponse pokhala ana a anthu Iye anapereka nyama za kuthengo, ndi mbalame za m'mlengalenga, m'dzanja lanu; nakucititsani ufumu pa izi zonse; inu ndinu mutuwo wagolidi.
39 Ndi pambuyo pa inu padzauka ufumu wina wocepa ndi wanu, ndi ufumu wina wacitatu wamkuwa wakucita ufumu pa dziko lonse lapansi.
40 Ndi ufumu wacinai udzakhala wolimba ngati citsulo, popeza citsulo ciphwanya ndi kufoketsa zonse; ndipo monga citsulo ciswa zonsezi, uwu udzaphwanya ndi kuswa.
41 Ndipo umo mudaonera mapazi ndi zala zace, mwina dongo la woumba, mwina citsulo; ufumuwo udzakhala wogawanika, koma momwemo mudzakhala mphamvu ya citsulo; popeza mudaona citsulo cosanganizika ndi dongo.
42 Ndi zala za mapazi, mwina citsulo ndi mwina dongo, momwemo ufumuwo, mwina wolimba mwina wogamphuka.
43 Ndi umo mudaonera citsulo cosanganizika ndi dongo, iwo adzadzisokoneza ndi ana a anthu wamba; koma sadzapharikizana, monga umo citsulo sicimasanganizikana ndi dongo.