15 Mukabvomereza tsono, pakumva mau a lipenga, citoliro, zeze, sansi, cisakasa, ndi ngoli, ndi zoyimbitsa ziri zonse, kugwadira ndi kulambira fano ndinalipanga, cabwino; koma mukapanda kulambira, mudzaponyedwa nthawi yomweyi m'kati mwa ng'anjo yotentha yamoto; ndipo mulungu amene adzakulanditsani m'manja mwanga ndani?
16 Sadrake, Mesake, ndi Abedinego, anayankha, nati kwa mfumu Nebukadinezara, Sikufunika kuti tikuyankheni pa mlandu uwu.
17 Taonani, Mulungu wathu amene timtumikira akhoza kutilanditsa m'ng'anjo yotentha yamoto, nadzatilanditsa m'dzanja lanu, mfumu.
18 Koma akapanda kutero, dziwani, mfumu, kuti sitidzatumikira milungu yanu, kapena kulambira fano lagolidi mudaliimikalo.
19 Pamenepo Nebukadinezara anadzazidwa ndi ukali, ndi maonekedwe a nkhope yace anasandulikira Sadrake, Mesake, ndi Abedinego; anayankha, nati asonkheze ng'anjo kasanu ndi kawiri koposa umo amasonkhezera.
20 Nauza amuna ena amphamvu a m'khamu lace la nkhondo amange Sadrake, Mesake, ndi Abedinego, ndi kuwaponya m'ng'anjo yotentha yamoto.
21 Pamenepo amuna awa anamangidwa ali cibvalire zopfunda zao, maraya ao, ndi nduwira zao, ndi zobvala zao zina; naponyedwa m'kati mwa ng'anjo yotentha yamoto.