12 Ndipo zirombo zotsalazo anazicotsera ulamuliro wao, koma anatalikitsa moyo wao, ukhalenso nyengo ndi nthawi.
13 Ndinaona m'masomphenya a usiku, taonani, anadza ndi mitambo ya kumwamba wina ngati mwana wa munthu, nafika kwa Nkhalamba ya kale lomwe; ndipo anamyandikizitsa pamaso pace.
14 Ndipo anampatsa ulamuliro, ndi ulemerero, ndi ufumu, kuti anthu onse, ndi mitundu yonse ya anthu, ndi a manenedwe onse, amtumikire; ulamuliro wace ndi ulamuliro wosatha wosapitirira, ndi ufumu wace sudzaonongeka.
15 Koma ine Danieli, mzimu wanga unalaswa m'kati mwa thupi langa, ndi masomphenya a m'mtima mwanga anandibvuta.
16 Ndinayandikira kwa wina wa iwo akuimako ndi kumfunsa za coonadi za ici conse. Ndipo ananena nane, nandidziwitsa kumasulira kwace kwa zinthuzi:
17 Zirombo zazikuru izi zinai ndizo mafumu anai amene adzauka pa dziko lapansi.
18 Koma opatulika la Wam'mwambamwamba adzalandira ufumuwo, ndi kukhala nao ufumu kosatha, ku nthawi zomka muyaya.