9 Ndinapenyerera mpaka anaikapo mipando yacifumu, nikhalapo Nkhalamba ya kale lomwe, zobvala zace zinali za mbu ngati cipale cofewa, ndi tsitsi la pa mutu pace ngati ubweya woyera, mpando wacifumu unali malawi amoto, ndi njinga zace moto woyaka.
10 Mtsinje wamoto unayenda woturuka pamaso pace, zikwi zikwi anamtumikira, ndi unyinji wosawerengeka unaima pamaso pace, woweruza mlandu anakhalapo, ndi mabuku anatsegulidwa.
11 Pamenepo ndinapenyera cifukwa ca phokoso la mau akuru idanena nyangayi; ndinapenyera mpaka adacipha ciromboci, ndi kuononga mtembo wace, ndi kuupereka utenthedwe ndi moto.
12 Ndipo zirombo zotsalazo anazicotsera ulamuliro wao, koma anatalikitsa moyo wao, ukhalenso nyengo ndi nthawi.
13 Ndinaona m'masomphenya a usiku, taonani, anadza ndi mitambo ya kumwamba wina ngati mwana wa munthu, nafika kwa Nkhalamba ya kale lomwe; ndipo anamyandikizitsa pamaso pace.
14 Ndipo anampatsa ulamuliro, ndi ulemerero, ndi ufumu, kuti anthu onse, ndi mitundu yonse ya anthu, ndi a manenedwe onse, amtumikire; ulamuliro wace ndi ulamuliro wosatha wosapitirira, ndi ufumu wace sudzaonongeka.
15 Koma ine Danieli, mzimu wanga unalaswa m'kati mwa thupi langa, ndi masomphenya a m'mtima mwanga anandibvuta.