10 sitinamvera mau a Yehova Mulungu wathu, kuyenda m'malamulo ace anatiikirawo pamaso pathu, mwa atumiki ace aneneri.
11 Inde Israyeli yense walakwira cilamulo canu, ndi kupambuka, kuti asamvere mau anu; cifukwa cace temberero lathiridwa pa ife, ndi Ilumbiro lolembedwa m'cilamulo ca Mose mtumiki wa Mulungu; pakuti tamcimwira.
12 Ndipo anakwaniritsa mau ace adanenawo, kutitsutsa ife ndi oweruza athu otiweruza, ndi kutitengera coipa cacikuru; pakuti pansi pa thambo lonse sipanacitika monga umo panacitikira Yerusalemu.
13 Monga mulembedwa m'cilamulo ca Mose coipa ici conse catidzera; koma sitinapepeza Yehova Mulungu wathu, ndi kubwera kuleka mphulupulu zathu, ndi kucita mwanzeru m'coonadi canu.
14 Cifukwa cace Yehova wakhala maso pa coipaco, ndi kutifikitsira ico; pakuti Yehova Mulungu wathu ali wolungama mu nchito zace zonse azicita; ndipo sitinamvera mau ace.
15 Ndipo tsopano, Ambuye Mulungu wathu, amene munaturutsa anthu anu m'dziko la Aigupto ndi dzanja lamphamvu, ndi kudzitengera mbiri monga lero lino, tacimwa, tacita coipa.
16 Ambuye, monga mwa cilungamo canu conse, mkwiyo wanu ndi ukali wanu zitembenuketu, zicoke ku mudzi wanu Yerusalemu, phiri lanu lopatulika; pakuti mwa zocimwa zathu, ndi mphulupulu za makolo athu, Yerusalemu ndi anthu anu asanduka cotonza ca onse otizungulira.