13 Monga mulembedwa m'cilamulo ca Mose coipa ici conse catidzera; koma sitinapepeza Yehova Mulungu wathu, ndi kubwera kuleka mphulupulu zathu, ndi kucita mwanzeru m'coonadi canu.
14 Cifukwa cace Yehova wakhala maso pa coipaco, ndi kutifikitsira ico; pakuti Yehova Mulungu wathu ali wolungama mu nchito zace zonse azicita; ndipo sitinamvera mau ace.
15 Ndipo tsopano, Ambuye Mulungu wathu, amene munaturutsa anthu anu m'dziko la Aigupto ndi dzanja lamphamvu, ndi kudzitengera mbiri monga lero lino, tacimwa, tacita coipa.
16 Ambuye, monga mwa cilungamo canu conse, mkwiyo wanu ndi ukali wanu zitembenuketu, zicoke ku mudzi wanu Yerusalemu, phiri lanu lopatulika; pakuti mwa zocimwa zathu, ndi mphulupulu za makolo athu, Yerusalemu ndi anthu anu asanduka cotonza ca onse otizungulira.
17 Ndipo tsopano, Mulungu wathu, mumvere pemphero la mtumiki wanu, ndi mapembedzero ace, nimuwalitse nkhope yanu pa malo anu opatulika amene ali opasuka, cifukwa ca Ambuye,
18 Mulungu wanga, cherani khutu, nimumvere, tsegulani maso anu, nimupenye zopasuka zathu, ndi mudzi udachedwawo dzina lanu; pakuti sititula mapembedzero athu pamaso panu, cifukwa ca nchito zathu zolungama, koma cifukwa ca zifundo zanu zocuruka.
19 Ambu ye, imvani; Ambuye, khululukirani; Ambuye, mverani nimucite; musacedwa, cifukwa ca inu nokha, Mulungu wanga; pakuti mudzi wanu ndi anthu anu anachedwa dzina lanu.