9 Ambuye Mulungu wathu ndiye wacifundo, ndi wokhululukira; pakuti tampandukira Iye;
10 sitinamvera mau a Yehova Mulungu wathu, kuyenda m'malamulo ace anatiikirawo pamaso pathu, mwa atumiki ace aneneri.
11 Inde Israyeli yense walakwira cilamulo canu, ndi kupambuka, kuti asamvere mau anu; cifukwa cace temberero lathiridwa pa ife, ndi Ilumbiro lolembedwa m'cilamulo ca Mose mtumiki wa Mulungu; pakuti tamcimwira.
12 Ndipo anakwaniritsa mau ace adanenawo, kutitsutsa ife ndi oweruza athu otiweruza, ndi kutitengera coipa cacikuru; pakuti pansi pa thambo lonse sipanacitika monga umo panacitikira Yerusalemu.
13 Monga mulembedwa m'cilamulo ca Mose coipa ici conse catidzera; koma sitinapepeza Yehova Mulungu wathu, ndi kubwera kuleka mphulupulu zathu, ndi kucita mwanzeru m'coonadi canu.
14 Cifukwa cace Yehova wakhala maso pa coipaco, ndi kutifikitsira ico; pakuti Yehova Mulungu wathu ali wolungama mu nchito zace zonse azicita; ndipo sitinamvera mau ace.
15 Ndipo tsopano, Ambuye Mulungu wathu, amene munaturutsa anthu anu m'dziko la Aigupto ndi dzanja lamphamvu, ndi kudzitengera mbiri monga lero lino, tacimwa, tacita coipa.