10 Tsiku lacisanu ndi ciwiri, pokondwera mtima wa mfumu ndi vinyo, iye anauza Mehumani, Bizita, Haribona, Bigita, ndi Abagita, Zetara, ndi Karikasi, adindo asanu ndi awiriwo akutumikira pamaso pa mfumu Ahaswero,
11 abwere naye Vasiti mkazi wamkuru pamaso pa mfumu ndi korona wacifumu, kuonetsa anthu ndi akuru kukoma kwace; popeza anali wokongola maonekedwe ace.
12 Koma Vasiti mkazi wamkuruyo anakana kudza pa mau a mfumu adamuuza adindowo; potero mfumu idapsa mtima ndithu, ndi mkwiyo wace unatentha m'kati mwace.
13 Pamenepo mfumu inanena kwa eni nzeru, akudziwa za m'tsogolo, mfumu idafotero nao onse akudziwa malamulo ndi maweruzo,
14 a pafupi naye ndiwo Karisena. Setara, Adimata, Tarisisi, Meresi, Marisena, ndi Memukana, akalonga asanu ndi awiri a Perisiya ndi Mediya, openya nkhope ya mfumu ndi kukhala oyamba m'ufumu.
15 Anati, Tidzacitanji naye mkazi wamkuru Vasiti monga mwa malamulo, popeza sanacita comuuza mfumu Ahaswero mwa adindo?
16 Ndi Memukana anati pamaso pa mfumu ndi akalonga, Vasiti mkazi wamkuru sanalakwira mfumu yekha, komanso akalonga onse, ndi mitundu yonse ya anthu okhala m'maiko onse a mfumu Ahaswero.