7 Ndinanenanso kwa mfumu, Cikakomera mfumu, indipatse akalata kwa ziwanga za tsidya lija la mtsinje, andilole ndipitirire mpaka ndifikira ku Yuda;
8 ndi kalata kwa Asafu wosunga misitu ya mfumu, kuti andipatse mitengo ya mitanda ya ku zipata, za linga liri kukacisi, ndi ya linga la mudzi, ndi ya nyumba imene ndidzalowamo ine. Ndipo mfumu inandipatsa monga mwa dzanja lokoma la Mulungu londikhalira.
9 Ndinafika tsono kwa ziwanga za tsidya lino la mtsinje, ndipo ndinawapatsa akalata a mfumu. Koma mfumu idatumiza apite nane akazembe a nkhondo, ndi apakavalo.
10 Atamva Sanibalati Mhoroni, ndi Tobiya kapoloyo M-amoni, cidawaipira kwakukuru, kuti wadza munthu kuwafunica ana a Israyeli cokoma.
11 Motero ndinafika ku Yerusalemu, ndi kukhalako masiku atatu.
12 Ndipo ndinauka usiku, ine ndi amuna owerengeka nane, osauza munthu yense ine coika Mulungu wanga m'mtima mwanga ndicitire Yerusalemu; panalibenso nyama yina nane, koma nyama imene ndinakhalapo.
13 Ndipo ndinaturuka usiku pa cipata ca kucigwa, kumka ku citsime ca cinjoka, ndi ku cipata ca kudzala, ndi kuyang'ana malinga a Yerusalemu adapasukawo, ndi zipata zace zothedwa ndi moto.