1 Ndipo kunali, atamva Sanibalati kuti tinalikumanga lingali, kudamuipira, nakwiya kwakukuru, naseka Ayuda pwepwete.
2 Nanena iye pamaso pa abale ace ndi ankhondo a ku Samariya, nati, Alikucitanji Ayuda ofokawa? adzimangire linga kodi? adzapereka nsembe kodi? adzatsiriza tsiku limodzi kodi? adzakometsanso miyala ya ku miunda yotenthedwa?
3 Ndipo Tobiya M-amoni anali naye, nati, Cinkana ici acimanga, ikakwerako nkhandwe, idzagamula linga lao lamiyala.
4 Imvani, Mulungu wathu, popeza tanyozeka ife; muwabwezere citonzo cao pamtu pao, ndi kuwapereka akhale cofunkhidwa m'dziko la ndende;
5 ndipo musakwirira mphulupulu yao, ndi kulakwa kwao kusafafanizike pamaso panu; pakuti anautsa mkwiyo wanu pamaso pa omanga linga.