1 Ndipo anthu onse anasonkhana ngati munthu mmodzi ku khwalala liri ku cipata ca kumadzi, namuuza Ezara mlembi atenge buku la cilamulo ca Mose, cimene Yehova adalamulira Israyeli.
2 Ndipo Ezara wansembe anabwera naco cilamulo pamaso pa msonkhano, ndiwo amuna ndi akazi, ndi yense wakumva ndi kuzindikira tsiku loyamba la mwezi wacisanu ndi ciwiri.
3 Nawerenga m'menemo pa khwalala liri ku cipata ca kumadzi kuyambira mbanda kuca kufikira msana, pamaso pa amuna ndi akazi, ndi iwo okhoza kuzindikira; ndi anthu onse anacherera khutu buku la cilamulo.
4 Ndipo Ezara mlembi anaima pa ciunda ca mitengo adacimangira msonkhanowo; ndi pambali: pace padaima Matitiya, ndi Sema, ndi Anaya, ndi Uriya, ndi Hilikiya, ndi Maaseya, ku dzanja lamanja lace; ndi ku dzanja lamanzere Pedaya, ndi Misayeli, ndi Malikiya, ndi Hasumu, ndi Hasibadana, Zekariya, ndi Mesulamu.
5 Ndipo Ezara anafunyulula bukulo pamaso pa anthu onse, popeza iye anasomphokera anthu onse; ndipo polifunyulula anthu onse ananyamuka.
6 Pamenepo Ezara analemekeza Yehova Mulungu wamkuru. Nabvomereza anthu onse, ndi kuti, Amen, Amen; nakweza manja ao, nawerama, nalambira Yehova nkhope zao pansi.