1 Ndipo tsiku la makumi awiri mphambu anai la mwezi uno ana a Israyeli anasonkhana ndi kusala, ndi kubvala ciguduli, ndipo anali ndi pfumbi.
2 Nadzipatula a mbumba ya Israyeli kwa alendo onse, naimirira, naulula zocimwa zao, ndi mphulupulu za makolo ao.
3 Naimima poima pao, nawerenga m'buku la cilamulo ca Yehova Mulungu wao limodzi la magawo anai a tsiku; ndi limodzi la magawo anai anaulula, napembedza Yehova Mulungu wao.
4 Pamenepo anaimirira pa ciunda ca Alevi Yesuwa, ndi Bani, Kadimiyeli, Sebaniya, Buni, Serebiya, Bani, ndi Kenani, napfuula ndi mau akuru kwa Yehova Mulungu wao.
5 Nati Alevi, Yesuwa, ndi Kadimiyeli, Buni, Hasabineya, Serebiya, Hodiya, Sebaniya, ndi Petatiya, Imirirani, lemekezani Yehova Mulungu wanu ku nthawi za nthawi; ndipo lilemekezeke dzina lanu la ulemerero, lokuzika loposa cilemekezo ndi ciyamiko conse.