1 Katundu wa mau a Yehova wakunena Israyeli.Atero Yehova, wakuyala miyamba, ndi kuika maziko a dziko lapansi, ndi kulenga mzimu wa munthu m'kati mwace;
2 Taonani, ndidzaika Yerusalemu akhale cipanda codzandiritsa kwa mitundu yonse ya anthu yozungulirapo, ndipo cidzafikira Yuda yemwe pomangira misasa Yerusalemu.
3 Ndipo kudzacitika tsiku ilo, ndidzaika Yerusalemu akhale mwala wolemetsa mitundu yonse ya anthu; onse akuusenza adzadzilasa nao; ndi amitundu onse a pa dziko lapansi adzasonkhana kutsutsana nao.
4 Tsiku ilo, ati Yehova, ndidzakantha kavalo ali yense ndi kumdabwitsa, ndi womkwera adzayaluka; ndipo ndidzatsegulira maso anga nyumba ya Yuda, ndi kukantha kavalo ali yense wa mitundu ya anthu akhale wakhungu.
5 Ndipo akalonga a Yuda adzanena m'mtima mwao, Okhala m'Yerusalemu ndiwo mphamvu yanga m'Yehova wa makamu Mulungu wao.
6 Tsiku ilo ndidzaika akalonga a Yuda ngati phale la moto pansi pa nkhuni, ndi ngati muuni wamoto mwa mitolo ya tirigu; ndipo adzatha mitundu yonse ya anthu pozungulirapo, ku dzanja lamanja ndi lamanzere; ndipo Yerusalemu adzakhalanso m'malo mwace, m'Yerusalemu.
7 Ndipo Yehova adzayamba kupulumutsa mahema a Yuda, kuti ulemerero wa nyumba ya Davide ndi ulemerero wa okhala m'Yerusalemu usakulire Yuda.