2 Ndipo ndinati, Upita kuti? Ndipo anati kwa ine, Kukayesa Yerusalemu, kuona ngati citando cace ncotani, ndi m'litali mwace motani.
3 Ndipo taonani, mthenga wolankhula nane anaturuka, ndi mthenga wina anaturuka kukomana naye,
4 nanena naye, Thamanga, lankhula ndi mnyamata uyu, ndi kuti, M'Yerusalemu mudzakhala anthu ngati m'midzi yopanda malinga, cifukwa ca kucuruka anthu ndi zoweta momwemo.
5 Pakuti Ine, ati Yehova, ndidzakhala kwa iye linga lamoto pozungulira pace, ndipo ndidzakhala ulemerero m'kati mwace.
6 Haya, haya, thawani ku dziko la kumpoto, ati Yehova; pakuti ndinakubalalitsani ngati mphepo zinai za kuthambo, ati Yehova.
7 Haya Ziyoni, thawa iwe wakukhala ndi mwana wamkazi wa Babulo.
8 Pakuti atero Yehova wa makamu: Utatha ulemererowo ananditumiza kwa amitundu amene anakufunkhani; pakuti iye wokhudza inu, akhudza mwana wa m'diso lace.